Here’s today’s lineup on Channel Africa, based on the official schedule:




Your favourite in one place — stay updated and in the running.
Enter exciting contests and giveaways. Stay tuned for chances to win exclusive Channel Africa merchandise and experiences.
Explore African rhythms, curated playlists, and artist spotlights from across the continent. Celebrate the sound of Africa with curated playlists.
Catch your favourite programs live or on-demand. From current affairs to cultural deep-dives, there’s something for every listener.
Listen to thought-provoking conversations, investigative series, and stories that matter — anytime, anywhere.
Your favourite in one place — stay updated and in the running.
The voices behind Channel Africa — passionate storytellers, journalists, and broadcasters from across the continent.
#Zochitika
Nkhani za masewera
>Bwalo loweluza za masewera padziko lonse, la Court of Arbitration for Sport, lati liyesetesa kupereka chigamulo pa pempho la dziko la Senegal mwachangu, atalandidwa chikho cha mpikisano wa Africa Cup of Nations (AFCON). Senegal inagonjetsa Morocco 1-0... mu ndime yomaliza pa 18 mwezi wa Januware, koma zotsatira zinasinthidwa Morocco kukhala yopambana ndi zigoli zitatu kwa ziro. Osewera a Senegal anachoka pabwalo la masewera pochita chiwonetsero pamene Morocco, yomwe inali yochititsa mpikisanowu, inapatsidwa penate mu nthawi yomaliza ya nthawi yowonjezera, koma pambuyo pake anabwerera kukamaliza masewerawo. Potsatira pempho la bungwe la Morocco Football Federation, bungwe la Confederation of African Football (CAF) linagamula kuti Senegal yataya masewerawo, ndipo zotsatira zidalembedwa ngati 3-0 mokomera Morocco.
>Kufunika kwa matikiti a mpikisano wa 2026 FIFA World Cup padziko lonse kwakwera kwambiri, ndipo okonda masewerawa apatsidwa mwayi womaliza kuti akatenge nawo gawo pa chikondwerero chachikulu cha mpira wamiyendo. Bungwe la FIFA latsimikiza kuti gawo lomaliza logulitsa matikiti la mphindi yotsiriza litsegulidwa lachitatu pa 1 mwezi wa Epulo. Matikiti adzagulitsidwa mwa njira ya amene wafika koyamba, pa tsamba la pa intaneti la FIFA.com. Zenera lomalizali logulitsira matikiti, likhala lotsegula mpaka kumapeto kwa mpikisano, kupatsa okonda masewerawa mwayi okhala mbali ya mbiri ya mpikisanowu.
>Desiree Ellis, mphunzitsi wamkulu wa timu ya azimayi ya mpira wamiyendo yadziko la South Africa, wati macheza ampira apaubale ndi timu ya Algeria, adzagwiritsidwa ntchito kupatsa mwayi kwa osewera akunja, pomwe kukonzekera kwa mpikisano wa Women's Africa Cup of Nations (WAFCON) kukupitilira. Mu gulu lake la osewera makumi awiri ndi anayi omwe akumane ndi Algeria pa 14 ndi pa 17 mwezi wa Epulo chaka chino, Ellis waphatikiziramo osewera atatu akunja odziwika bwino, Amogelang Motau amene amasewera ndi timu ya Club Tijuana yamdziko la Mexico, Hilda Magaia wa timu ya Deportivo La Coruna yamdziko la Spain, ndi Linda Motlhalo wa Glasgow City yamdziko la Scotland. Polankhula ndi gawo la SABC lowulutsa za masewera, Ellis watsindika kufunika kophatikiziranso osewera omwe amasewera kunja......
>Njira yokapezera malo mu mpikisano wa CAF Africa Cup of Nations PAMOJA 2027 yayamba lero ndi masewera a chipulula, pomwe matimu khumi ndi awiri akupikisana kuti apeze malo asanu ndi amodzi omwe alipo kuti apite ku gawo lotsatira. Eritrea inakumana ndi Eswatini dzulo ku Meknes mdziko la Morocco komwe Eritrea yapambana ndi zigoli ziwiri kwa ziro, ndipo masewera akabwereza achitikira mdziko la Eswatini lachiwiri sabata yamawa. Lesotho ndi Seychelles anakumana mdera la Free State mdziko la South Africa nthawi ya 4 koloko madzulo a lero, ndipo alepherana 0-0, kenako adzakumanso pa bwalo lomwelo patatha masiku atatu. Djibouti ndi South Sudan anakuma nthawi ya 3 koloko madzulo alero, Djibouti yakwapulidwa 4-0, ndipo masewera onse awiri achitikira pa bwalo la Juba mdziko la South Sudan. Mawali, Somalia idzakumana ndi Mauritius pa masewera oyamba mtauni ya Matola mdziko la Mozambique, ndipo achiwiri adzachitikira pa National Sports Complex mu mzinda wa Saint Pierre mdziko la Mauritius pa 31 mwezi omwe uno. Chad ndi Burundi ayamba nkhondo yawo yopitira ku mpikisanowu pa bwalo la Stade Olympique mu mzinda wa N'Djemena mawa nthawi ya 3 koloko madzulo, ndipo achiwiri mu mzinda wa Bujumbura masiku anayi otsatira. Sao Tome and Principe ikumana ndi Ethiopia mawa nthawi ya 6 koloko madzulo mu mzinda wa El Jadida, ndipo masewera achiwiri adzakhala mu mzinda wa Dire Diwa mdziko la Ethiopia pa 31 mwezi omwe uno.
>Mlembi wa Unduna wa Zachinyamata ndi Zamasewera mdziko la Kenya, Salim Mvurya, wati akugwira ntchito mosalekeza kuti alipire ndalama zokwana 29 miliyoni dollars zomwe zikufunika kuti achititse mpikisano wa chaka chamawa wa Africa Cup of Nations (AFCON). Mchikalata, Mvurya wati pali mgwirizano wapamwamba womwe ukupitilirabe kuwonetsetsa kuti ndalama zolipira ziperekedwe pa nthawi yake kuti dzikolo lipewe manyazi. Undunawo wati ukugwira ntchito limodzi ndi nkhokwe ya za chuma yadzikolo, komanso Nyumba ya Malamulo, kuti athane ndi zachuma zomwe zikuyembekezeka kudzera mu mndondomeko yowonjezera ya bajeti, kuwonetsetsa kuti akupita patsogolo ndikukonzekera. Mantha anayamba sabata yatha pamene Mlembi wamkulu wa zamasewera, Elijah Mwangi, anauza Nyumba ya Malamulo kuti dzikolo silinapereke ndalama zolipira kuti lichititse mpikisanowu, pomwe kwatsala masiku osapitilira masabata awiri kuti tsiku lomaliza lifike pa 30 mwezi wa Marichi.
Alex Nkhuku
Channel Africa News.
#ZOCHITIKA
MU NKHANI ZATHU ZA CHUMA
#Unduna wa zaulimi mdziko la Malawi, wati pomwe pamafika pa 13 Marichi, alimi okwana 925,428 anali atagula zipangizo zaulimi zotsika mtengo m'dzikolo kuimila 85% zomwe ati zasiyana ndi momwe zidalili chaka chatha pomwe nthawi ngati yomwe ...67% yaalimi ndi womwe adali atapindula mu ndondomekoyi.
Mu mwezi wa Octobala chaka chatha, mtsogoleri wadzikolo Professor Arthur Peter Mutharika adauza mtundu wa a Malawi kuti chiwerengero cha anthu opindula ndi ndondomeko yi chikwera kuchoka pa 530,000 kufika pa anthu 1.1 million.
Malingana ndi nduna ya za ulimi mdzikolo, Roza Mbilizi, bungwe la international fund for agricultural Development (IFAD) lidathandiza-po pa ndondomekoyi ndi ma tani afeteleza okwana 2,200 komanso ma tani a mbewu okwana 110.
#Bungwe loteteza ma ufulu a anthu pa malonda mdziko la South Africa, la National Consumer Commission of South Africa, lati kuitanitsa kwa magalimoto a mtundu wa Ford Transit and Toureno, kukuphatikiza ma batire omwe anaikidwa mmagalimotowa. Bungweli, laitanitsa magalimotowa kuchokera kwa makatsomala omwe anagula magalimotowa poona kuti pali kuthekera kopangitsa ngozi, monga kutentha kwa mabatire, mwa zina. Oyendetsa magalimotowa, athanso kumava fungo kuchokera mkati mwa magalimotowa komanso kununkha mphweya wa gasi.
#Nduna za malonda zochokera mmaiko a mu Africa, zikukumana mdziko la Cameroon pomwe zikukambirana nkhani zofuna kuunikira mwa ndondomeko zina zokhudza bungwe la World Trade Organisation. Mkumanowu, ndi wa masiku anayi, ndipo wadza pa nthawi yomwe maiko maka mu Africa akudandaula pa nkhani yokhudza mikangano yomwe ikuchitika ku chigawo cha aluya, komanso misonkho yomwe presidenti wa dziko la USA Donald Trump anakhazikitsa pa malonda ochokera mmaiko angapo.
Thamo Kapisa
Channel Africa News
#ZOCHITIKA
NKHANI ZATHU ZA LERO PA CHINYANJA SERVICE
#Bungwe loona za anthu othawa kwawo la IOM, lati anthu asanu ndi anayi amawalira pamene ena okwana 45 akusowa potsatira bwato lomwe anakwera kumira mu mphepete mwa nyanja mdziko la Djibouti. Malingana ndi lipoti lochokera mu ...bungwe la United Nations, ngoziyi inachitika pa 24 Marichi, ndipo bwatoli linanyamula anthu okwana 320. Pakadali pano, sizikudziwika kuti bwatoli linachokera pa doko liti komanso kuti limafuna kukafika kuti. Mmiyezi yapitayi, ma bwato akhala akumira mu mphepete mwa nyanja mdzikoli komanso ku maiko ena monga a Libya, potsatira anthu kukwera mwa bwato osabvomelezeka omwe ali ndi cholinga chofuna kukafikitsa anthu ku ulaya. Bungwe la IOM, lati chiwerengero cha anthu omwe anamwalira pa ngozi za kumira kwa ma bwato, chinali pa 922 chaka chatha.
#Presidenti wa dziko la South Africa Cyril Ramaphosa, wati agwira ntchito limodzi ndi yemwe akugwirizira mpando wa nduna yoona zintchito za apolisi, Firoz Cachalia, pa kufuna kuonetsetsa kuti zintchito mu undunawu zisasokonezedwe. Ramaphosa, walankhula motere potsatira bungwe lozenga milandu mmalo mwa boma la National Prosecuting Authority, dzulo kupereka ma summon kwa komishonala wa unduna wa apolisi, Gen Fannie Masemola, komanso kumangidwa kwa akulu akulu ena mu undunawu okwana khumi ndi awiri.
Pakadali pano, bungweli silinapereke ndondomeko wa milandu yomwe Masemola akuzengedwa.
#Dziko la Israel, lati lapha mkulu oona zintchito za bungwe la asilikali mdziko la Iran, lotchedwa Iran Revolutionary Guard. Izi, ndi malinga ndi nduna yoona za chitetezo mdziko la Israel, Israel Katz, yemwe wati Alireza Tangsiri, waphedwa potsatira boma kuphulitsidwa, pomwe akulu akulu ena mu bungweli aphedwa. Katz, wati Tangsiri, ndi yemwe amapangitsa kuti doko la Strait of Hormuz lidzikaniza kudutsitsa mabwato ena omwe anyamula katundu maka mafuta. Dziko la Iran, silinabwere poyera ndi kutsindika za imfa ya Tangsiri. Mtolankhani wa BBC, Frank Gardner, wafotokoza kunena kuti mikangano ikupitilira, ndipo madera ku aluya monga a Gulf, Kuwait, Saudi Arabia komanso UAE, akupitilira kuponyeledwa mabomba.
#Mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma m'nyumba ya malamulo mdziko la Malawi, Simplex Chithyola Banda wauza nyumbayi kuti chipani cha MCP chapanga ganizo kuti sichitenga nawo mbali mu kafukufuku watsopano wa ngozi ya ndege yemwe nyumbayi ikufuna kuchita.
Mukuyankha kwake, sipikala wanyumbayi, Sameer Suleman wati aikirapo ndemanga yake pa ganizo la chipanichi.
A Chithyola Banda, anena izi kutsatira kuwulutsidwa kwa mndandanda wa anthu omwe akhale mu komiti yapaderayi umene sipikala wa nyumba ya malamulo a Sameer Suleman analengeza mnyumbayi omwe mamembala anayi a chipani cha DPP, awiri a MCP, zipani za UTM, UDF ndi PP membala mmodzimodzi, pomwe oima pa okha munali mamembala atatu.
Kunali mtsutso pa nkhani ya anthu omwe awaika mu komitiyi pamene a MCP amati sipikala wachotsa dzina la phungu wawo mmodzi a Monica Chang'anamuno pa mndandanda wa anthu okhala mu komitiyi pomwe chipanichi chimayenera kukhala ndi mamembala atatu osati awiri.
Pa zokambiranazi, phungu wa Nkhotakota Central a Silvester Ayuba James ati akukhulupilira kuti anthu onse omwe adayankhulapo zokhudza ngoziyi mmbuyomu, samayenera kukhalamo, monga a Felix Njawala a mchipani cha UTM.
#Yemwe anachotsedwa pa mpando ngati presidenti wa dziko la Venezuela, Nicholas Maduro, yemwe pakadali pano ali mmanja mwa dziko la USA, pamodzi ndi mkazi wake, akuyembekezeka kuonekera pa bwalo la milandu mma ora akubwerawa mu mzinda New York. Aka, kakhala kachiwiri Maduro ndi mkwazi wake, Celia Flores, kuonekera mu bwaloli, potsatira kugwidwa ndi asilikali a boma la dziko la USA mu mwezi wa Januare chaka chino, kuti akayankhe milandu yokhudza zida za nkhondo, komanso uchigawenga, kapena kuti terrorism pa chingerezi.
Thamo Kapisa
Channel Africa News
UNHRC ati nkhaza zosiyanasiyana zikuwonjezeka kamba kakumenyana mdziko la South Sudan #Zochitika
Join Mariamo Hassamo on #Caleidoscopio – a News and Current Affairs show that provides the latest updates on major news stories.
The show covers breaking stories as we round up all the news events of the day, especially on the African Continent between 20:00 – 21:00 CAT
...#ChannelAfrica
Muli bwanji Africa.
Ndi nthawi ya #Zochitika ndi Mada Phiri.
Fikani kuti mukhale mukudziwa zomwe zikuchitika mu Africa ndi padziko lonse lapansi.
#ChannelAfrica
Mada Phiri hosts you on #Zochitika - a News and Current Affairs show that provides the latest updates on major news stories.
The show covers breaking stories as we round up all the news events of the day, especially on the African Continent between 19:00 – 20:00 CAT.
...#ChannelAfrica
Subscribe to our newsletter and stay informed with the latest news, program highlights, and exclusive content from Channel Africa — a trusted voice in global broadcasting.
Channel Africa promotes Africa’s national interests through innovative content aiding the continent’s development. We deliver news, current affairs, and cultural programming globally, broadcasting in multiple languages to connect Africa to the world and the world to Africa.